Table Of ContentMtanthauziramawu wa Chinyanja
Published by the Centre for Language Studies
A
A, a1 /k/ dzi. Mu-A- (zambi. ma a)
lembo loyamba mu mndandanda wa malembo a m’chiyankhulo cha
Chichewa ndiponso limodzi la malembo asanu aliwu: a, e, i, o, u.
a2 dzi. Mu-A- (zambi. ma a)
mawu osonyeza ulemu potchula dzina la munthu. lero kuli mowa kwa a
Chintengo
aa1 /k/ mfu.
mawu osonyeza kudabwa, kutsutsa, kapena kusakondwa ndi zochitika. aa!
zatero? aa! ine sindinali nawo
aa2 /k/ mfu.
mawu onena poinga nkhuku, mbalame ndi zina. anafuula kuti ‘aa! aa!’
kuinga nkhuku zomwe zinali kujompha ufa.
abakadya /ttkt/ dzi. Mu-A (zambi. abakadya)
chilonda chosapola mpaka imfa kapena chilonda chamgonagona. anayesa
kuthira mankhwala osiyanasiyana pa chilondacho kuti chipole koma
chifukwa chosachisamalira bwino chinasanduka abakadya
abee /tk/ mfu.
mawu amene akazi amanena povomera kuitanidwa. pamene Maliya
adamuyitana amake adavomera kuti ‘abee’
abwito /tkt/ dzi. Mu-A- (zambi. abwito)
tinthu tonga mafinya totuluka m’maso chakumphepete (manthongo).
nditadzuka m’mawa, ndinapita kukasukusula kumaso pofuna kuchotsa
abwito
achale (Nge) /kt/ Mu-A- (zambi. achale)
chakudya chokometsera ndiwo chopangidwa posakaniza tsabola wambiri
ndi zipatso monga mango, anyezi ndi adyo. amwenye ambiri amakonda
kudya zakudya zatsabola wambiri monga achale
adakulasa dzi. Mu-A- (zambi. adakulasa)
kagulu ka nyenyezi zisanu ndi ziwiri zowala bwino. mae.: msangwe,
akamwiniatsatana, mauta. atayang’ana kumwamba, adachita chidwi ndi
kagulu ka nyenyezi kowala kwambiri ndipo agogo ake adamuwuza nyenyezi
zotero amazitcha adakulasa
adiresi (Nge) dzi. I-zi- (zambi. adiresi)
dzina la malo amene munthu amakhala. mae.: keyala. ndimati mundipatse
adiresi yanu kuti ndidzakulembereni kalata ndikadzafika kumudzi.
adyo /kt/ Mu-A- (zambi. adyo)
mtundu wa chomera chokhala ndi thima loyerera ndi masamba obiriwira
motuwira chafungo lamphamvu chomwe anthu amakometsera chakudya
makamaka ndiwo. fani: anyezi. pitani kumsika kukagula adyo kuti
tidzathire ndiwo
aironi (Nge) /kt/ dzi. I-Zi- (zambi. aironi)
chipangizo chomwe amayikamo moto wamakala kapena wamagetsi ndi
kumasitira zovala. mae.: simbi. a Phiri anayika moto wamakala mu aironi
kuti asite zovala zawo.
akamwiniatsatana /tkkkt/ dzi. Mu-A- (zambi. akamwiniatsatana)
onani tanthauzo la adakulasa
akutsano1 /tk/ dzi. Mu-A- (zambi. akutsano)
1 amake a mfumu. a Nasimango monga akutsano obereka mfumu
Chinkombero analandira ulemu woposa pa mwambo wolonga mfumuyi
2 mkazi wa mfumu. a Namulauzi, omwe tsopano akwatiwa ndi mfumu,
anawalangiza kuti iwo monga akutsano ayenera kukhala munthu
woyanjanitsa anzawo.
akwaa /tk/ mfu.
mawu osonyeza kudabwa, kukhumudwa ndi zochitika. mae.: ekwee, asaa,
alaa. akwaa! monga mwana uja wamwaliradi.
alaa /tk/ mfu.
onani tanthauzo la akwaa.
aleluya (Heb) /ttkt/ mfu.
aleluya ndi mawu otanthawuza ‘lemekezani Yehova. ’. tikondwere! pamene
mwana anapulumuka pa ngozi yowopsayo, tonse tinafuula mwachimwemwe
kuti ‘aleluya!’
Allah (Arab) /kt/ dzi. Mu-A- .
Allah ndi mawu omwe anthu achipembedzo chachisilamu amatchulira
Mulungu. pamene anasonkhana ku msikiti, asilamu anathokoza Allah
chifukwa cha zabwino zomwe amawachitira.
alumali /ttkt/ dzi. Mu-A- (zambi. alumali)
tsanja loyikapo zinthu makamaka zogulitsa m’sitolo kapena m’golosale. a
Phiri anagula katundu wa m’sitolo mwawo ndipo anamusanja pa alumali
kuti makasitomala awo azitha kumuwona bwino.
alungu dzi. Mu-A- (zambi. alungu)
1 mizimu ya anthu akufa. mae.: amanda. 2 maloto kapena masomphenya
momwe anthu amaona anthu akufa. usiku ndalota alungu akundiwuza uti
ana amasiyewa tiziwasamala ngati athu omwe
amanda1 Mu-A- (zambi. amanda)
onani tanthauzo 1 la alungu
amanda2 dzi. Mu-A- (zambi. amanda)
mtundu wa mpunga womwe umakhala wonunkhira kwambiri. alimi ambiri
a kudera la nyanja ya Chirwa amakonda kubzala mpunga wa amanda.
ambulasi (Nge) dzi. (zambi. ambulasi)
galimoto lomwe limakhala ndi zipangizo zapadera lomwe limatenga
munthu wodwala kapena wovulala kupita naye ku chipatala. matenda
atakula, dokotala wa pachipatala chaching’ono anayitanitsa ambulasi kuti
itenge wodwalayo kupita naye kuchipatala chachikulu.
ambulera (Nge) /tkkt/ dzi. I-Zi- (zambi. ambulera)
ambulera ndi chinthu chopangidwa ndi nsalu yoterera yokungidwa ndi
chokhala ndi chigwiriro chomwe anthu amafunda podziteteza ku mvula
kapena dzuwa. dzulo kunali mvula yambiri ndipo ndinanyowa chifukwa
ndinalibe ambulera
ambwana (Sho) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. ambwana)
mawu oyitanira anthu olingana msinkhu kutanthauza mnzanga. mae.: ayise,
bwanawe, mwaiwe. ambwana, tiye tizipita kunyumba popeza kunjaku
kwada.
ame (Heb) mfu.
mawu omwe akhirisitu amanena potsiriza pemphero kapena nyimbo
kutanthauza kuti ‘kukhale choncho. ’. atatsiriza pemphero lopempherera
wogwalayo, onse anayankha kuti ‘ame. ’.
andiroko (Afr) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. andiroko)
chovala cham’kati chonga siketi chomwe amavala akazi. andiroko ya
Nabiyeni yabooka choncho wapita kwa telala kukasoketsa. .
anyezi (Nge) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. anyezi)
mtundu wa chomera chonga adyo chafungo la mphamvu koma losiyana ndi
la adyo, chokometsera chakudya makamaka ndiwo. pitani kumsika
mukagule anyezi kuti tidzathire ndiwo.
apiro (Nge) dzi. I-Zi-
pempho limene munthu amapereka kwa mkulu woweruza milandu kuti
mlandu wake wa munthu wopemphayo ukaweruzidwe ku khoti lina
lapamwamba chifukwa chosakhutira ndi momwe khoti loyambalo
laweruzira mlanduwo. khoti linagamula kuti mlondayo amangidwe zaka
zisanu chifukwa chopezeka ndi mlandu wakuba koma iye sanakhutitsidwe
ndi chigamulochi choncho anachita apiro ku khoti lalikulu.
asa /tk/ mfu.
onani tanthauzo la akwaa. asa! bwanji mukuchita phokoso pamene anzanu
akuwerenga?
asi /tk/ muo.
mawu osonyeza kukana. kunekwi.: ashi. mae.: ayi. asi, sindipita kuphwando
la ukwati popeza ndikudwala.
asikolo /kt/ (Nge) I-Zi- (zambi. asikolo)
chitsulo kapena thabwa loikamo magalasi lomwe amamangirira ku feremu
la zenera. kunekwi.: atikolo. pamene amamanga nyumba anayika asikolo ya
magalasi asanu ndi limodzi pa zenera la chipinda cha ana.
atulo /ttk/ dzi. Mu-A- (zambi. atulo)
maganizo odza mwa munthu pamene ali mtulo ndipo zinthu za
m’maganizozo zimakhala ngati zoona. mae.: maloto. usiku wathawu amayi
akhalira kubwebweta, atulo awavuta kwambiri.
ayata /tkt/ dzi. Mu-A- (zambi. ayata)
mphini zomwe akazi amatema m’matako ndi m’ntchafu. chinali
chizolowezi cha akazi akale kutema mphini za ayata m’ntchafu ndi
m’matako.
ayi /tk/ muo.
onani tanthauzo la asi. ayi, sindipita kuphwando la ukwati popeza
ndikudwala.
ayise /ttk/ dzi. (Nge)
onani tanthauzo la ambwana. ayise, tiye tizipita kunyumba popeza kunjaku
kwada.
ayisikirimu (Nge) /kkt/ dzi. Mu-A- (zambi. ayisikirimu)
chakudya chozuna chopanga posakaniza shuga, mkaka ndi zinthu zina za
ufa monga kasitadi. ana ambiri amakonda kudya zakudya zotsekemera
monga ayisikirimu.
ayo /kt/ mfu.
mawu osonyeza kudandaula chifukwa cha chisoni kapena kupweteka kwa
m’thupi. mae.: koto!, mayo! anali kubuula kuti ‘ayo!’, ‘ayo!’ pamene thupi
linali kuwaphwanya.
B
B, b dzi. Mu-A- (zambi. ma b)
lembo lachiwiri mu mndandanda wa malembo a chiyankhulo cha Chichewa
ndipo ndi limodzi mwa malembo opanda liwu khumi, mphambu zisanu ndi
zinayi
ba1 /k/ mve.
1 ‘ba’ ndi umo limamvekera phokoso la khasu pokumba pansi pouma
kapena phokoso la chitseko potseka mwamphamvu. anamenyetsa chitseko
kuti ba panthawi imene anali kuthamangitsa mbala
2 ‘ba’ ndi momwe chimaonekera chinthu chikamatulukira pabwalo kapena
pakhomo mwadzidzidzi. antchito onse anadzidzimuka bwana atangoti ba
mmawa kwambiri pa ofesipo.
ba2 Ku-, mne.
tenga chinthu cha mwini chomwe sichili chako mozembetsa. mae. : njonja,
psasa.
baa /tk/ mfu.
mawu amene amamveka ng’ombe ikamalira. pamene ng’ombeyo
inabayidwa pakhosi inalira kuti ‘baa!’.
baba1 /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. ababa)
1 dzina limene mwana amayitanira atate ake. baba, ndimapempha kuti
mukandigulire malaya.
2 dzina loitanira munthu aliyense wamkulu, wamwamuna. kodi mwaswera
bwanji baba?
baba2 Ku-, mne.
funa kumwa madzi kapena zinthu zina zamadzimadzi. atayenda ulendo
wautali padzuwa anamva kubaba choncho anapempha madzi kuti amwe.
babada Ku-, mne.
menya pamutu kapena pafupa ndi chinthu monga ndodo. kunekwi.: boboda.
mae.: babadula. aphunzitsi anababada pamutu ophunzira onse ochita
phokoso.
babadira Ku-, mne.
New entry. seems to have the same meaning as badira below.
babaika /tttk/ Ku-, mne.
kayika pochita chinthu. chifukwa choti anali kubabaika pogula katunduyo,
munthu wina wachangu anagula katundu yenseyo kuwasiya iwo
akudandaula.
babaiza Ku-, mne.
phimba chinthu china pa chovala chosakwanira kapena choperewera. siketi
yomwe anavala inali yayifupi choncho anababaiza ndi chitenje.
babakula Ku-, mne.
lowetsa mimba m’kati pakanthawi pokokera mpweya mkati. mae.: bakhula,
befula, defula, fenkhula, nenkhula, kalima. consider: tamula mimba
pakanthawi pokokera mpweya mkati. munthu wodwala chibayo amavutika
kubabakula popeza m’thiti mwake mumapweteka.
babanyira Ku-, mne.
onani tanthauzo la babadira.
bada muo.
khala wopanda zovala m’thupi. mae.: buno, maliseche, mbulanda, psata,
popeza anali ndi malaya amodzi komanso kabudula mmodzi ndiye
akachapa amangokhala bada osavala kanthu.
bade dzi. Li-Ma- (zambi. mabade)
fupa la mutu lomwe limatchinjiriza bongo. kunekwi.: chibade. mae.:
dambe, nkhadzi, nkhatho, chibada, chigadza. munthu wokwera mthuthuthu
amavala chisoti choteteza bade la mutu wake pa ngozi.
badira Ku-, mne.
konza mtanda wa nsima m’sengwa kapena m’mbale ndi chipande kuti
uoneke wosalala. mae.: babanyira.
badwa Ku-, mne.
tuluka m’mimba mwamayi pachiyambi cha moyo. kodi mwana wanu
anabadwa chaka chanji?
badza dzi. Li-Ma- (zambi. mabadza)
chikho kapena chinthu chilichonse champhako monga bango chomaeta
nemba mbali imodzi m’kumaimba povina gule wamganda kapena
malipenga. povina gule wamalipenga anthu amayimba chipangizo
chotchedwa badza.
bafa (Nge) dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. bafa/mabafa)
1 malo osambiramo. agogo anagwa kubafa pamene anali kusamba.
2 chiwiya chosambiramo. madziwo akafunda muwakhutulire mu bafa.
bafuta /tkt/ dzi. I-Zi- (zambi. bafuta)
mtundu wa nsalu yoyera,. yolimba koma yofewa ndiponso yoterera ngati
mafuta. panthawi yolongedwa ufumu, amwale anavala mkanjo wa nsalu
yabafuta.
baibulo (Nge) /kt/ dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. baibulo/mabaibulo)
Bukhu Lopatulika la mawu a Mulungu. iwo amakonda kuwerenga baibulo
tsiku lililonse madzulo asanagone.
baji (Nge) dzi. I-Zi-/Li-Ma- (zambi. baji/mabaji)
chizindikiro chachinthu chilichonse choika pachovala monga pa jekete
kapena malaya. iye amakonda kuvala baji ya chipani chake posonyeza
kuchinyadira.
bakha Mu-A- (zambi. abakha)
mbalame yoweta yonga tsekwe yokonda kusambira m’madzi ndipo mapazi
ake ndi olukanalukana. bambo wanga amakonda kudya nyama yabakha
bakha dzi. Mu-A- (zambi. abakha)
mbalame yoweta yonga tsekwe yokonda kusambira m’madzi ndipo
mapadzi ake ndi olukanalukana. bambo anga anapha bakha wonona dzulo.
bakhalibakhali mve.
umo amaonekera munthu kapena chinthu chikamachita chinthu mofulumira
ndi mwaliwiro. anthu amachita bakhalibakhali nthawi yakummawa
kuthamangira kuntchito zawo zosiyanasiyana.
bakhula Ku-, mne.
onani tanthauzo la babakula. munthu wodwala chibayo amavutika
kubabakhula popeza m’thiti mwake mumapweteka.
bala1 Ku-, mne.
1 tulutsa mwana kuchoka m’mimba monga amachitira munthu kapena
nyama yaikazi. mbuzi yanga ija yabala mwana wakufa.
2 khala ndi zipatso monga imachitira mitengo. mae. : patsa. mtengo
waukulu uja wabala mango ambiri chaka chino.
3 chita mabulu kapena undana monga umachitira ufa m’madzi ogaduka
pokandira nsima. pepani nsimayi ili ndi mabulu popeza phala linabala
panthawi yokandira.
bala2 /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabala)
malo amene atemedwa pakhungu mwatsopano apa. anali ndi bala
pamwendo chifukwa galu anamuluma.
bala3 (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabala)
malo ogulitsira ndi kumwerako mowa. amalume anali ndi matsire choncho
anapita kubala kuti akamwe mowa.
balala /k/ mve.
umo zimaonekera zinthu zikakhala momwazika kapena mong’ondoka.
mae.: ng’ondo. itabuka ndewu mumsikamo malonda ambiri anatsakamuka
ndipo anangoti balala ponseponse.
balalika /tttk/ Ku-, mne.
khala momwazika monga chimanga chikatayika. consider: choka pamalo
kupita mbali zosiyanasiyana malinga ndi komwe aliyense wachokera.
msonkhano utatha anthu onse anabalalika kupita kwawo.
balamanthu mve.
umo amaonekera munthu kapena chinthu chikatulukira kapena kuonekera
poyera mwadzidzidzi. mae.: buchi, tulukiru. alenje anayamba kuthawa
mkango utangoti balamanthu.
balang’ombe dzi. Li-Ma- (zambi. mabalang’ombe)
mavu akuluakulu akuda. mae mphang’ombe, chiphang’ombe, bavunyondo,
chidazi. nkhope yake inatupa atalumidwa ndi mavu abalang’ombe.
balani (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabalani)
nyumba yotchisiramo fodya. fodya wawo anawonongeka ndi mvula
chifukwa balani yomwe amatchisiramo inali yothonya.
balasuku (Pwi) dzi. Li-Ma- (zambi. mabalasuku)
chidutswa chagalasi losweka. galasilo litaswanyika anasesa mabalasuku
onse kuopa kuti anthu angawaponde ndi kubaidwa.
balaula dzi. Mu- A- (zambi. abalaula)
kachilombo kamtundu wagulugufe kokhala ndi mapiko anayi akuluakulu
oyerera kapena amawangamawanga. mae.: pherupheru, chiphepheru. ndi
kovuta kusiyanitsa gulugufe ndi balawula popeza tizilombo tiwiriti
timafanana kwambiri.
balawu dzi. Mu-A- (zambi. abalawu)
nkhumba yaikulu yaimuna. popeza kuti anali ndi nkhumba zazikazi
zokhazokha anapita kwa achimtengo kukabwereka balawu kuti nkhumba
zawozo zikhale ndi bere.
balaza (Swa) /tkt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabalaza)
chipinda chochezeramo. kunekwi.: balanda. timakonda kucheza pa balaza
ya nyumba yathu tsiku lililonse pambuyo pachakudya cha madzulo.
bale (Nge) /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. bale)
mtundu wa fodya wamasamba ataliatali yemwe amamuwumitsa ndi dzuwa.
chaka chamawa ndidzalima fodya wa bale kuti ndidzapeze ndalama
zambiri.
bama Ku-, mne.
kumba pansi polimba ndi khasu kapena piki. kunekwi.: bamantha. mae.:
bamanthula. khasu linabuntha pobama dzenje lotayamo zinyatsi.
bambala dzi. Li-Ma- (zambi. mabambala)
mpanda wozungulira khola la nkhumba kuti zisamatuluke. mae.: gwekwe.
anamanga bambala la mitengo ya malaina pofuna kuti nkhumba zawo
zisamatuluke.
bambi /tk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabambi)
mbali yaifupi ya chinthu monga nsalu. kunekwi.: bwambi. mae.: lifupi.
nsalu yomwe anagula inali yamamita asanu mu litali ndi mamita awiri mu
bambi.
bambo dzi. Mu-A- (zambi. abambo)
1 kholo lalimuna. bambo wanga amagwira ntchito ku Lilongwe.
2 mwamuna aliyense wamkulu bambo akupita apowo akuyenda ngati
aledzera.
3 wansembe wamipingo ina monga Katolika ndi Angilikani. akulu ampingo
anapita kutchalitchi kukawadziwitsa bambo za kumwalira kwa mmodzi wa
akhirisitu.
bampala (Nge) /kt/ dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. bampala/mabampala)
chitsulo cha galimoto chokhala mopingasa kutsogolo kapena kumbuyo
kwake chotchinjiriza galimoto ku zinthu zomwe ingagunde. galimoto ziwiri
zitagundana, galimoto imodzi inaonongeka injini popeza bampala yake
inali yosalimba.
banda /tk/ dzi. I-Zi- (zambi. banda)
mtundu wa nyerere zokulirapo zonga ndandu zomwe zili ndi miyendo
italiitali. mwana anayamba kulira pamene banda zinamukwera pamwendo
koma amake anamusasa mwa nsanga nyererezo.
bandakula Ku-, mne.
chotsa chotsekera cha pamphika, botolo kapena bokosi. mae. vundukula,
funthukhula. ndiwozo zitabwata, anabandakula chivindikiriro kuti athire
nchere.
bandali /ttk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabandali)
malo amene nyanja yalowa ku mtunda. mae.: nsolomondo, ndomo. alimi
amabvala mbewu zosiyanasiyana mphepete mwa bandali makamaka madzi
akasefukira.
bandawe /kt/ dzi. Mu-A- (zambi. abandawe)
mtundu wa chimanga chimene chili ndi chitsononkho chooneka ngati
chadyedwa ndi chiswe. mae.: kachiswe. bungwe la Admarc laonjeza kuti
chaka chino lidzagula kwa alimi chimanga cha mtundu wa bandawe
chomwe chimatchedwanso kuti kachiswe.
bande /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mawande)
1 njira yowanda pa thengo. mae.: chikuwa. apolisi anapeza katundu yemwe
mbala zinabisa m’tchire potsatira bande lomwe mbalayo inadzera pokabisa
katunduyo.
2 mtundu wa udzu womera m’mbali mwa nyanja kapena mwa mtsinje.
anamanga msasa wa udzu wa bande kuti azigonamo pamene anapita
kukagula nsomba kwa asodzi kunyanja.
bandeji (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabandeji)
kansalu komangira chilonda kapena malo opweteka. atanditsuka
chilondacho ndi kuthirapo mankhwala, dokotala anandimanga bandegi
pofuna kuti fumbi lisalowe pachilondacho.
bandi (Nge) /kt/ dzi. I-Zi-/ Li-Ma- (zambi. bandi/mabandi)
gulu la anthu oimba ndi zipangizo zoimbira moonga malipenga, zitoliro,
gitala, ng’oma ndi zina. anthu anasangalala povina ku ukwati wa Mavuto
ndi Chimwemwe chifukwa kunali bandi yodziwa kuyimba.
bandira Ku- mne.
1 kwezera dothi pathumbira polima munthu akatha kupalira mbewu. mae.:
chimbanda. kubandira mbewu ndi kofunika ngakhale kuti nthawi zina
kumapangitsa kuuti mbewuzo zidyedwe ndi chiswe chifukwa cha dothi
lokwezedwalo.
2 samba pa dziwe mwapholoso pochita nsambi. mnzanga anamira pa dziwe
ilo chifukwa chosadziwa kubandira.
bandu /tk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabandu)
gawo limodzi la chinthu chathunthu likadulidwa monga dzungu. kunekwi.:
chibandu. anandipatsa bandu la dzungu kuti ndidye koma sindinakhute.
banduka Ku- mne.
thamanga mofulumira kwambiri. dilayivala anachita ngozi pa gulaye
chifukwa anali kubanduka kwambiri.
bandula Ku-, mne.
1 waza chinthu cholimba monga nsungwi. mae.: walula. tengani thabwa
lija kuseriko mubandule kuti tichite nkhuni.
2 consider: menya. amene akundinena ine ndimubandula mpaka atuluke
magazi.
banga dzi. Li-Ma- (zambi. mawanga)
dontho la mtundu wina monga pa thupi la nyama kapena pa nsalu. mae.:
thotho. chitenje chomwe amayi agula chili ndi banga la chikasu pakati.
bango /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mawango)
chomera chonga udzu cha makwaule ataliatali osongoka chimene anthu
amasoka mphasa ndipo chimamera m’mbali kapena mu mtsinje. bwato
lomwe amapalasa litagadama, maliko anapulumuka osamira chifukwa
anagwira bango m’mbali mwa mtsinjewo.
bango /tk/ dzi. Li-Ma- (zambi. mango)
chipatso chamtengo wamango chomwe chokhala ndi nthangala yaikulu
yoyera m’kati mwake. mae.: lingo, yembe. mango akakhala aawisi
amawawasa ndipo amakhala bwino kususira ndi mchere ndi tsabola.
bangula /ttk/ Ku-, mne.
1 lira monga momwe umachitira mkango. mae.: uluma, luluma. alenje
anayamba kuthawa pamene anamva kubangula kwa mkango.
2 fuula ndi mawu aakulu ndiponso amphamvu. pamene anapsa mtima,
anayamba kubangula chifukwa cha ukali
bangwe dzi. Mu- A- (zambi. abangwe)
chipangizo choimbira chokhala ndi nsambo zisanu ndi ziwiri chomwe
chimafana kwambiri ndi gitala. kunekwi.: pangwe. mae.: pango. nsambo
zina za bangwe wake zinali zosakungika choncho sanali kumveka bwino.
bani (Nge) /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. mabani)
chakudya chofanana ndi sikono chopangidwa ndi ufa wa tirigu. iye anali
ndi njala koma pamene anadya bani mkumwera madzi, mtima wake
unatsika.
banika /ttk/ Ku-, mne.
leka kupuma kwa kanthawi pang’ono. mnyumbamo munali utsi wambiri
kotero kuti anthu anayamba kubanika koma anayamba kupuma bwino
atatsegula mazenera.
banja /kt/ dzi. Li-Ma- (zambi. maanja)
1 mwamuna ndi mkazi wake. Mavuto ndi Chimwemwe anamanga banga
chaka chatha.
2 maanja angapo otuluka nyumba m’banja limodzi. ?